Amos 5:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake zimene akunena Chauta, Ambuye, Mulungu Wamphamvuzonse, ndi izi: “M'mabwalo monse mudzakhala kulira, ndipo m'miseu monse anthu azidzangoti, ‘Mayo! Mayo!’ Ngakhale anthu wamba adzaŵaitana kuti adzalire, adzaitananso anthu odziŵa kubuma maliro kuti adzalire.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake atero Yehova, Mulungu wa makamu, Ambuye, M'makwalala onse mudzakhala kulira, ndi m'miseu yonse adzati, Kalanga ine! Kalanga ine! Nadzaitana wakumunda adze kumaliro, ndi odziwa maliridwe a nthetemya alire.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho izi ndi zimene Ambuye, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, akunena: “Mʼmisewu monse mudzakhala kulira mofuwula, ndi kulira chifukwa cha kuwawa kwa masautso kudzakhala paliponse. Adzayitana alimi kuti adzalire, ndipo anthu odziwa maliridwe anthetemya adzalira mofuwula.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace atero Yehova, Mulungu wa makamu, Ambuye, M'makwalala onse mudzakhala kulira, ndi m'miseu yonse adzati, Kalanga ine! kalanga ine! nadzaitana wakumunda adze kumaliro, ndi odziwa maliridwe a nthetemya alire.