Amos 5:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kudzakhala monga m'mene kumachitira munthu akamathaŵa mkango, ndipo akumana ndi chimbalangondo, kapena monga munthu woti wakaloŵa m'nyumba, atsamira chipupa ndi dzanja lake, njoka nkumuluma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kudzakhala monga munthu akathawa mkango, ndi chimbalangondo chikomana naye; kapena akalowa m'nyumba, natsamira kukhoma ndi dzanja lake, nimluma njoka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Lidzakhala ngati tsiku limene munthu pothawa mkango amakumana ndi chimbalangondo, ngati pamene munthu walowa mʼnyumba, natsamira dzanja lake pa khoma ndipo njoka nʼkuluma.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kudzakhala monga munthu akathawa mkango, ndi cimbalangondo cikomana naye; kapena akalowa m'nyumba, natsamira kukhoma ndi dzanja lace, nimluma njoka.