Amos 5:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimene akunena Ambuye Chauta ndi izi: “Mzinda umene udapita ku nkhondo ndi anthu chikwi udzatsala ndi anthu zana limodzi chabe. Ndipo umene udapita ku nkhondo ndi anthu zana limodzi, udzatsala ndi anthu khumi okha a m'banja la Israele.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti atero Ambuye Yehova, M'nyumba ya Israele, mudzi wotulukamo chikwi chimodzi adzautsalira zana limodzi, ndi uwu wotulukamo zana limodzi adzautsalira khumi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ambuye Yehova akuti, “Mzinda umene udzapite ku nkhondo ndi anthu 1,000 amphamvu udzatsala ndi anthu 100 okha; mzinda umene udzapite ku nkhondo ndi anthu 100 amphamvu udzatsala ndi anthu khumi okha basi.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti atero Ambuye Yehova, M'nyumba ya Israyeli, mudzi woturukamo cikwi cimodzi adzautsalira zana limodzi, ndi uwu woturukamo zana limodzi adzautsalira khumi.