Amos 5:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muchite zimene Chauta afuna, kuti mukhalebe ndi moyo. Mukapanda kutero, adzatentha banja la Yosefe ngati moto, ndipo motowo udzapsereza a ku Betele popanda wina wouzimitsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Funani Yehova, ndipo mudzakhala ndi moyo; angabuke ngati moto m'nyumba ya Yosefe, ndipo unganyeke wopanda wakuzima m'Betele;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Funani Yehova kuti mukhale ndi moyo, mukapanda kutero Iye adzatentha nyumba ya Yosefe ngati moto; motowo udzawononga, ndipo sipadzakhala wina wozimitsa motowo ku Beteli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Funani Yehova, ndipo mudzakhala ndi mayo; angabuke ngati moto m'nyumba ya Yosefe, ndipo unganyeke wopanda wakuzima m'Beteli;