Amos 5:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iye uja ndiye amene adalenga nyenyezi za Akamwiniatsatana ndiponso Nsangwe, ndiye amene amasandutsa mdima kuti ukhale m'maŵa nasandutsa usana kuti ukhale usiku. Ndiye amene amaitana madzi am'nyanja ndi kuŵathira pa dziko lapansi. Dzina lake ndi Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iye wakulenga Nsangwe ndi Akamwiniatsatana, nasanduliza mdima wandiweyani ukhale m'mawa, nasanduliza usana ude ngati usiku, wakuitana madzi a m'nyanja, nawatsanulira pa dziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
(Iye amene analenga nyenyezi za Nsangwe ndi Akamwiniatsatana, amene amasandutsa mdima kuti ukhale mmawa ndi kudetsa usana kuti ukhale usiku, amene amayitana madzi a mʼnyanja ndi kuwathira pa dziko lapansi, Yehova ndiye dzina lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iye wakulenga Nsangwe ndi Akamwiniatsatana, nasanduliza mdima wandiweyani ukhale m'mawa, nasanduliza usana ude ngati usiku, wakuitana madzi a m'nyanja, nawatsanulira pa dziko lapansi, dzina lace ndiye Yehova;