Amos 6:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsoka kwa inu amene mumakhala mosatekeseka ku Ziyoni, ndiponso kwa inu amene mumakhala mosavutika ku Samariya. Tsoka kwa inu anthu otchuka pakati pa Aisraele, inu amene anthu onse amafika kwanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsoka osalabadirawo m'Ziyoni, ndi iwo okhazikika m'phiri la Samariya, ndiwo anthu omveka a mtundu woposa wa anthu, amene nyumba ya Israele iwafikira!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsoka kwa amene simukulabadira kanthu ku Ziyoni, ndiponso kwa inu amene mukukhala mwamtendere pa Phiri la Samariya, inu anthu otchuka ochokera ku mtundu wa anthu omveka, kumene Aisraeli amafikako!
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsoka osalabadirawo m'Ziyoni, ndi iwo okhazikika m'phiri la Samariya, ndiwo anthu omveka amtundu woposa wa anthu, amene nyumba ya Israyeli iwafikira!