Amos 6:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mbale wake wa wina mwa akufawo, woyenera kusamala za maliro, adzafika kudzatulutsa mtembo m'nyumbamo. Tsono adzafunsa wina amene watsalakobe m'nyumbamo kuti, “Kodi uli ndi winanso wamoyo m'menemo?” Iyeyo adzayankha kuti, “Ai mulibiretu.” Ndipo mbaleyo adzati, “Khala chete, iwe! Tisayerekeze kutchula dzina la Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mbale wake wa munthu akamnyamula, ndiye womtentha, kutulutsa mafupa m'nyumba, nakati kwa iye ali m'kati mwa nyumbamo, Atsala wina nawe kodi? Nakati Iai; pamenepo adzati, Khala chete; pakuti sitingatchule dzina la Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo ngati mʼbale wake wa wina wakufayo, woyenera kusamala za maliro, adzafika kudzatulutsa mitembo mʼnyumbamo nʼkufunsa aliyense amene akubisalabe mʼnyumbamo kuti, “Kodi uli ndi wina wamoyo mʼmenemo?” Ndipo munthu wobisalayo ndi kuyankha kuti, “Ayi,” mʼbaleyo adzanena kuti, “Khala chete! Ife tisayerekeze kutchula dzina la Yehova.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mbalewace wa munthu akamnyamula, ndiye womtentha, kuturutsa mafupa m'nyumba, nakati kwa iye ali m'kati mwa nyumbamo, Atsala wina nawe kodi? nakati, lai; pamenepo adzati, Khala cete; pakuti sitingachule dzina la Yehova.