Amos 6:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kodi pa thanthwe akavalo nkuthamangapo? Kodi panyanja wina nkulimapo ndi ng'ombe? Komabe chilungamo mwachisandutsa chivumulo, ndipo zaungwiro mwazisandutsa zoŵaŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi akavalo adzathamanga pathanthwe? Kodi adzalimako ndi ng'ombe pakuti mwasanduliza chiweruzo chikhale ndulu, ndi chipatso cha chilungamo chikhale chivumulo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kodi akavalo amathamanga pa thanthwe? Kodi wina amatipula ndi ngʼombe mʼnyanja? Koma chiweruzo cholungama mwachisandutsa kukhala zinthu zakupha ndipo chipatso cha chilungamo mwachisandutsa kukhala chowawa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi akavalo adzathamanga pathanthwe? kodi adzalimako ndi ng'ombe? pakuti mwasanduliza ciweruzo cikhale ndulu, ndi cipatso ca cilungamo cikhale civumulo;