Amos 6:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukunyadira kuti mudagonjetsa mzinda wa Lodebara, mukunena kuti, “Kodi suja tidapambana mzinda wa Karinaimu ndi mphamvu zathu zokha?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
inu okondwera nacho chopanda pake, ndi kuti, Kodi sitinadzilimbitsa tokha ndi kulanda Karinaimu mwa mphamvu yathuyathu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu amene mukunyadira kuti munagonjetsa Lo Debara ndipo mukunena kuti, “Kodi sitinatenge Karinaimu ndi mphamvu zathu zokha?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
inu okondwera naco copanda pace, ndi kuti, Kodi sitinadzilimbitsa tokha mwa mphamvu yathu yathu?