Amos 6:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse akuti, “Ndidzakuputirani anthu a mtundu wina kuti adzakuthireni nkhondo, inu Aisraele. Adzakuzunzani kuyambira ku Mpata wa Hamati kumpoto mpaka ku mfuleni wa Araba kumwera.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti taonani, ndidzakuutsirani mtundu wa anthu, nyumba ya Israele, ati Yehova Mulungu wa makamu; ndipo adzakupsinjani kuyambira polowera ku Hamati kufikira mtsinje wa kuchidikha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma Yehova Mulungu Wamphamvuzonse akulengeza kuti, “Inu nyumba ya Israeli, ndidzakudzutsirani mtundu wina wa anthu umene udzakuzunzani kuchokera ku Lebo Hamati mpaka ku Chigwa cha Araba.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti taonani, ndidzakuutsirani mtundu wa anthu, nyumba ya Israyeli, ati Yehova Mulungu wa makamu; ndipo adzakupsinjani kuyambira polowera ku Hamati kufikira mtsinje wa kucidikha.