Amos 6:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pitani ku mzinda wa Kaline mukaone. Mupitenso ku Hamati mzinda wotchuka uja, tsono mutsikire ku Gati kwa Afilisti. Kodi Aisraelenu mukupambana anthu a mafumu ameneŵa? Kodi kapena dziko lao nlalikulu kupambana lanu?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pitani ku Kaline, nimuone; kuchokera komweko mupite ku Hamati wamkulu mutsikire ku Gati wa Afilisti; kodi awo ndi okoma koposa maufumu ano? Kapena malire ao aposa malire anu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pitani ku mzinda wa Kaline mukawuyangʼane; mukapitenso ku Hamati-raba mzinda waukulu uja, ndipo mukatsikirenso ku Gati kwa Afilisti. Kodi mizinda imeneyi ndi yopambana maufumu anu awiriwa? Kodi dziko lawo ndi lalikulu kupambana lanu?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pitani ku Kaline, nimuone; kucokera komweko mupite ku Hamati wamkulu mutsikire ku Gati wa Afilisti; kodi awo ndi okoma koposa maufumu ano? kapena malire ao aposa malire anu?