Amos 6:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsoka kwa inu amene mumagona pa mabedi oŵakongoletsa ndi minyanga yanjovu, inu amene mumangoti lamzi pa mipando yanu, nkumachita phwando la nyama ya anaankhosa osakhwima ndi ya anaang'ombe onenepa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ogona pamakama aminyanga, nadzithinula pa maguwa ao ogonapo, nadya anaankhosa a kuzoweta, ndi anaang'ombe ochoka pakati pa khola;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mumagona pa mabedi owakongoletsa ndi minyanga ya njovu, mumagona pa mipando yanu ya wofuwofu. Mumadya ana ankhosa onona ndi ana angʼombe onenepa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ogona pa makama aminyanga, nadzithinula pa maguwa ao ogonapo, nadya ana a nkhosa a ku zoweta, ndi ana a ng'ombe ocoka pakati pa khola;