Amos 6:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ambuye Chauta alumbira m'dzina lao kuti, “Ndikunyansidwa ndi zimene ana a Yakobe akunyadira, ndikudana nazo nyumba zao zazikulu. Ndithu ndidzapereka kwa adani ao likulu lao ndi zonse zam'menemo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ambuye Yehova walumbira pali Iye mwini, ati Yehova Mulungu wa makamu, Ndinyansidwa nako kudzikuza kwa Yakobo, ndidana nazo nyumba zake zachifumu; m'mwemo ndidzapereka mudzi, ndi zonse zili m'menemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ambuye Yehova walumbira mʼdzina lake. Yehova Mulungu Wamphamvuzonse walengeza kuti, “Ndimanyansidwa ndi kunyada kwa Yakobo, ndimadana ndi nyumba zake zaufumu; Ine ndidzawupereka mzindawu pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ambuye Yehova walumbira pali Iye mwini, ati Yehova Mulungu wa makamu, Ndinyansidwa nako kudzikuza kwa Yakobo, ndidana nazo nyumba zace zacifumu; m'mwemo ndidzapereka mudzi, ndi zonse ziri m'menemo.