Amos 7:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ku Betele kunali wansembe wina dzina lake Amaziya. Iyeyo adatumiza mthenga kwa Yerobowamu, mfumu ya ku Israele kuti, “Amosi akukuutsirani chiwembu pakati pa anthu a ku Israele. Anthu sangathe kuvomera zonse zimene iye akunenazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo Amaziya wansembe wa ku Betele anatumiza kwa Yerobowamu mfumu ya Israele, ndi kuti, Amosi wapangira inu chiwembu pakati pa nyumba ya Israele; dziko silikhoza kulola mau ake onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamenepo Amaziya wansembe wa ku Beteli anatumiza uthenga kwa Yeroboamu mfumu ya Israeli kuti, “Amosi akukuutsirani chiwembu pakati pa Aisraeli. Dziko silingalekerere zonena zake zonsezo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo Amaziya wansembe wa ku Beteli anatumiza kwa Yerobiamu mfumu ya Israyeli, ndi kuti, Amosi wapangira inu ciwembu pakati pa nyumba ya Israyeli; dziko silikhoza kulola mau ace onse.