Amos 7:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Nchifukwa chake tsono imva mau amene Chauta akunena. Iweyo ukundiwuza kuti ndisalose zotsutsa Israele, ndisalalike zotsutsa banja la Isaki.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake tsono, tamvera mau a Yehova, Iwe ukuti, Usamanenera chotsutsana ndi Israele, usadonthetsa mau akutsutsana ndi nyumba ya Isaki;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono imva mawu a Yehova. Iwe ukunena kuti, “ ‘Usanenere zotsutsa Israeli, ndipo siya kulalikira motsutsa nyumba ya Isake.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace tsono, tamvera mau a Yehova, Iwe ukuti, Usamanenera cotsutsana ndi Israyeli, usadonthetsa mau akutsutsana ndi nyumba ya Isake;