Amos 7:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono zimene akunena Chauta ndi izi: ‘Mkazi wako adzasanduka mkazi wadama mumzindamu. Ndipo ana ako aamuna ndi aakazi adzaphedwa pa nkhondo. Dziko lako adzaligaŵagaŵa kugaŵira anthu ena. Iweyo ukafera ku dziko lachikunja. Ndipo Aisraele adzatengedwa kunka ku ukapolo kutali ndi dziko lao.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
chifukwa chake atero Yehova, Mkazi wako adzakhala wadama m'mudzi, ndi ana ako aamuna ndi aakazi adzagwa ndi lupanga, ndi dziko lako lidzagawanidwa ndi kuyesa chingwe, ndi iwe mwini udzafa m'dziko lodetsedwa; ndipo Israele adzatengedwadi ndende kuchoka m'dziko lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsono zimene akunena Yehova ndi izi: “ ‘Mkazi wako adzasanduka wachiwerewere mu mzindamu, ndipo ana ako aamuna ndi aakazi adzaphedwa ndi lupanga. Munda wako udzayezedwa ndi chingwe ndi kugawidwa, ndipo iwe mwini udzafera mʼdziko la anthu osapembedza Mulungu. Ndipo Israeli adzatengedwa ndithu kupita ku ukapolo, kutali ndi dziko lake.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
cifukwa cace atero Yehova, Mkazi wako adzakhala wadama m'mudzi, ndi ana ako amuna ndi akazi adzagwa ndi lupanga, ndi dziko lako lidzagawanidwa ndi kuyesa cingwe, ndi iwe mwini udzafa m'dziko lodetsedwa; ndipo Israyeli adzatengedwadi ndende kucoka m'dziko lace.