Amos 7:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene ndidaona kuti dzombelo ladya zomera zonse zam'dzikomo, ndidati, “Inu Ambuye Chauta, ndapota nanu, khululukani. Kodi anthu a Yakobeŵa angalimbike bwanji? Iwoŵa ndi ofooka kwambiri.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunachitika m'mene lidatha kudya msipu wa dziko, ndinati, Ambuye Yehova, khululukiranitu Yakobo; adzakhala chilili bwanji? Popeza ndiye wamng'ono.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dzombelo litadya zomera zonse za mʼdzikomo, Ine ndinafuwula kuti, “Ambuye Yehova, khululukani! Kodi Yakobo adzapulumuka bwanji? Iye ndi wofowoka kwambiri!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunacitika m'mene lidatha kudya msipu wa dziko, ndinati, Ambuye Yehova, khululukiranitu Yakobo; adzakhala ciriri bwanji? popeza ndiye wamng'ono.