Amos 7:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zina ndi izi zimene Ambuye Chauta adandiwonetsa m'masomphenya: Ambuye Chauta ankaitana malaŵi a moto kuti alange anthu. Motowo udapsereza phompho lalikulu, nuyamba kuwononga minda yonse ya pa dziko lapansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ambuye Yehova anandionetsa chotere; ndipo taonani, Ambuye Yehova anaitana kuti atsutse ndi moto; ndipo unanyambita chakuya chachikulu ukadanyambitanso dziko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zimene Ambuye Yehova anandionetsa ndi izi: Ambuye Yehova ankayitana malawi a moto kuti alange anthu. Motowo unawumitsa nyanja yakuya ndi kupsereza dziko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ambuye Yehova anandionetsa cotere; ndipo taonani, Ambuye Yehova anaitana kuti atsutse ndi moto; ndipo unanyambita cakudya cacikuru ukadanyambitanso dziko.