Amos 8:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zikondwerero zanu ndidzazisandutsa kulira, nyimbo zanu ndidzazisandutsa zamaliro. Ndidzakuvekani chiguduli nonsenu pathupi panu, ndipo mitu yanu yonse idzachita dazi. Mudzakhala ngati anakubala olira mwana wao mmodzi yekha. Tsiku limenelo lidzakhaladi loŵaŵa mpaka kutha kwake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzasanduliza zikondwerero zanu zikhale maliro, ndi nyimbo zanu zikhale za maliro, ndi kufikitsa ziguduli m'chuuno monse, ndi mpala pa mutu uliwonse; nadzakhala ngati maliro a mwana mmodzi yekha, ndi chitsiriziro chake ngati tsiku lowawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Maphwando anu achipembedzo ndidzawasandutsa kulira kwa chisoni ndipo kuyimba kwanu konse ndidzakusandutsa maliro. Ndidzakuvekani chiguduli nonsenu ndi kumeta mipala mitu yanu. Nthawi imeneyo idzakhala ngati yolira mwana wamwamuna mmodzi yekhayo, ndipo tsikulo lidzakhala lowawa mpaka kutha kwake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzasanduliza madyerero anu, akhale maliro, ndi nyimbo zanu zikhale za maliro, ndi kufikitsa ziguduli m'cuuno monse, ndi mpala pa mutu uli wonse; nadzakhala ngati maliro a mwana mmodzi yekha, ndi citsiriziro cace ngati tsiku lowawa.