Amos 8:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onse amene amalumbira m'dzina la Asima, mulungu wa Samariya, nkumanena kuti, ‘Pali mulungu wa ku Dani!’ Kapena kuti, ‘Pali njira yopatulika ya ku Beereseba!’ Onsewo adzagwa osadzukanso.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iwo akulumbira ndi kutchula tchimo la Samariya, ndi kuti, Pali Mulungu wako, Dani; ndipo, Pali moyo wa njira ya ku Beereseba, iwowa adzagwa, osaukanso konse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Onse amene amalumbira pa tchimo la Samariya, kapena kumanena kuti, ‘Iwe Dani, pali mulungu wako wamoyo,’ kapena, ‘Pali mulungu wamoyo wa ku Beeriseba.’ Iwowo adzagwa ndipo sadzadzukanso.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iwo akulumbira ndi kuchula cimo la Samariya, ndi kuti, Pali Mulungu wako, Dani; ndipo, Pali moyo wa njira ya ku Beereseba, iwowa adzagwa, osaukanso konse.