Amos 8:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta adandifunsa kuti, “Kodi iwe Amosi, nchiyani ukuwonachi?” Ine ndidayankha kuti, “Dengu la zipatso zakupsa.” Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Nthaŵi ya chimalizo yaŵakwanira anthu anga Aisraele, sindidzaŵakhululukiranso.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati, Amosi uona chiyani? Ndipo ndinati, Dengu la zipatso zamalimwe. Nati Yehova kwa ine, Chitsiriziro chafikira anthu anga Israele, sindidzawalekanso.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anandifunsa kuti, “Amosi nʼchiyani ukuona?” Ine ndinayankha kuti, “Dengu la zipatso zakupsa.” Ndipo Yehova anati kwa ine, “Nthawi yachimaliziro yawakwanira anthu anga Aisraeli; sindidzawakhululukiranso.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati, Amosi uona ciani? Ndipo ndinati, Mtanga wa zipatso zamalimwe. Nati Yehova kwa ine, Citsiriziro cafikira anthu anga Israyeli, sindidzawalekanso.