Amos 8:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nyimbo za m'Nyumba ya Mulungu zidzasanduka kulira pa tsiku limenelo. Mitembo ya anthu idzachuluka, ndipo adzaiponya ponseponse. Kudzangoti zii!” Akuterotu Ambuye Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma nyimbo za ku Kachisi zidzasanduka kubuma tsiku ilo, ati Ambuye Yehova; mitembo idzachuluka; adzaitaya paliponse padzakhala zii.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsiku limenelo,” Ambuye Yehova akulengeza kuti, “Nyimbo za mʼNyumba ya Mulungu zidzasanduka kulira kofuwula. Mitembo ya anthu idzachuluka, ndipo adzayiponya ponseponse! Kudzangoti zii!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma nyimbo za kukacisi zidzasanduka kubuma tsiku ilo, ati Ambuye Yehova; mitembo idzacuruka; adzaitaya pali ponse padzakhala zii.