Amos 8:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu mumadzifunsa kuti, ‘Kodi chikondwerero cha kukhala kwa mwezi chidzatha liti, kuti tigulitse dzinthu? Kodi tsiku lopumula la Sabata litha liti kuti tigulitsenso tirigu, kutinso tipeze mpata wochepetsera miyeso ndi kukweza mitengo, ndiponso kuti tichenjeretse anthu ndi masikelo onama,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwezi wokhala upita liti, kuti tigulitse dzinthu? Ndi Sabata, kuti titsegulire tirigu? Ndi kuchepsa efa, ndi kukulitsa sekeli, ndi kuchenjerera nayo miyeso yonyenga;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mumanena kuti, “Kodi chikondwerero cha mwezi watsopano chidzatha liti kuti tigulitse zinthu? Ndipo tsiku la Sabata litha liti kuti tigulitse tirigu, kuti tichepetse miyeso, kukweza mitengo kuti tibere anthu ndi miyeso ya chinyengo,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwezi wokhala upita liti, kuti tigulitse dzinthu? ndi Sabata, kuti titsegulire tirigu? ndi kucepsa efa, ndi kukuliitsa sekeli, ndi kucenjerera nayo miyeso yonyenga;