Amos 9:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ndidaona Chauta ataima pambali pa guwa. Adati, “Gwetsani makapotolosi a Nyumba ya Mulungu, kuti maziko ake agwedezeke. Muŵagwetsere pamitu pa anthu. Onse otsalira Ine ndidzaŵapha pa nkhondo. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzathaŵe. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzapulumukepo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndinaona Ambuye alikuima pa guwa la nsembe, nati Iye, Kantha mitu ya nsanamira, kuti ziundo zigwedezeke; nuphwanye mitu yao yonse; ndipo ndidzapha otsiriza ao ndi lupanga; wothawayo mwa iwo sadzathawadi, ndi wopulumukayo mwa iwo sadzapulumukadi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndinaona Ambuye atayima pambali pa guwa lansembe, ndipo anati: “Kantha mitu ya nsanamira kuti ziwundo za nyumba zigwedezeke. Muzigwetsere pa mitu ya anthu onse, onse amene atsalira ndidzawapha ndi lupanga. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzathawe, palibe amene adzapulumuke.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndinaona Ambuye alikuima pa guwa la nsembe, nati Iye, Kantha mitu ya nsanamira, kuti ziundo zigwedezeke; nuphwanye mitu yao yonse; ndipo ndidzapha otsiriza ao ndi lupanga; wothawayo mwa iwo sadzathawadi, ndi wopulumukayo mwaiwosadzapulumukadi.