Amos 9:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akuti, “Nthaŵi imeneyo ndidzakwezanso ufumu wa Davide umene udagwa ngati nyumba. Ndidzakonzanso makoma ake ogumuka ndi kumanganso mabwinja ake. Ndidzaubwezeranso mwake mwakale.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsiku lomwelo ndidzautsa msasa wa Davide udagwawo, ndi kukonzanso zopasuka zake; ndipo ndidzautsa zogumuka zake, ndi kuumanga monga masiku a kalelo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsiku limenelo ndidzabwezeretsa nyumba ya Davide imene inagwa. Ndidzakonzanso malo amene anagumuka, ndi kuyimanganso monga inalili poyamba,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsiku lomwelo ndidzautsa msasa wa Davide udagwawo, ndi kukonzanso zopasuka zace; ndipo ndidzautsa zogumuka zace, ndi kuumanga monga masiku a kalelo;