Amos 9:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta akunena kuti, “Nthaŵi ikubwera pamene mlimi adzabzola wokolola, ndipo woponda mphesa adzabzola wobzala mbeu. M'mapiri mudzatuluka vinyo wokoma, azidzachita kuyenderera pa zitunda zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Taonani, akudza masiku, ati Yehova, akuti wolima adzapezana ndi wodula, ndi woponda mphesa adzapezana ndi wofetsa, ndi mapiri adzakhetsa vinyo watsopano, ndi zitunda zonse zidzasungunuka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova akunena kuti “Nthawi ikubwera pamene mlimi wotipula adzapyola wokolola ndipo woponda mphesa adzapyola wodzala mbewu. Mapiri adzachucha vinyo watsopano ndi kuyenderera pa zitunda zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Taonani akudza masiku, ati Yehova, akud wolima adzapezana ndi wodula, ndi woponda mphesa adzapezana ndi wofesa, ndi mapiri adzakhetsa vinyo watsopano, ndi zitunda zonse zidzasungunuka.