Amos 9:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ndidzaŵabwezeranso pabwino anthu anga Aisraele. Adzamanganso mizinda yamabwinja ndi kumakhalamo. Adzalima minda ya mphesa ndipo adzamwa vinyo wake. Adzalima minda ndipo adzadya zipatso zake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzabwezanso undende wa anthu anga Israele, ndipo adzamanganso mabwinja, ndi kukhala m'menemo; nadzaoka minda ya mipesa nadzamwa vinyo wake, nadzalima minda ndi kudya zipatso zake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndidzawabwezeranso pabwino anthu anga Aisraeli; mizinda imene inali mabwinja idzamangidwanso ndipo azidzakhalamo. Adzalima minda ya mpesa ndipo adzamwa vinyo wake; adzalima minda ndipo adzadya zipatso zake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzabwezanso undende wa anthu anga Israyeli, ndipo adzamanganso mabwinja, ndi kukhala m'menemo; nadzaoka minda ya mipesa nadzamwa vinyo wace, nadzalima minda ndi kudya zipatso zace.