Amos 9:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ngakhale akabisale pamwamba pa phiri la Karimele, ndidzaŵaunguza nkuŵagwira. Ngakhale akabisale pansi pa nyanja yaikulu, ndidzalamula chilombo cham'nyanjamo kuti chiŵalume.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Angakhale abisala pamwamba pa Karimele, ndidzawapwaira ndi kuwatenga komweko; angakhale abisala pamaso panga pansi pa nyanja, kumeneko ndidzalamulira njoka, ndipo idzawaluma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale atakabisala pamwamba pa phiri la Karimeli, Ine ndidzawasaka kumeneko ndi kuwagwira. Ngakhale atakabisala pansi pa nyanja yayikulu, ndidzalamula njoka kuti iwalume kumeneko.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Angakhale abisala pamwamba pa Karimeli, ndidzawapwaira ndi kuwatenga komweko; angakhale abisala pamaso panga pansi pa nyanja, kumeneko ndidzalamulira njoka, ndipo idzawaluma.