Amos 9:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ambuye Chauta Wamphamvuzonse, akakhudza dziko, limanyenyeka, ndipo zonse zokhala m'menemo zimalira. Apo dziko lonse limafufuma ngati mtsinje wa Nailo ndipo limateranso ngati mtsinje wa Nailo wa ku Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Ambuye Yehova wa makamu ndiye amene akhudza dziko, nilisungunuka; ndi onse okhalamo adzachita maliro; ndipo lidzakwera lonseli ngati madzi a m'nyanja; nilidzatsikanso ngati nyanja ya m'Ejipito;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ambuye Yehova Wamphamvuzonse amene amakhudza dziko lapansi ndipo dzikolo limasungunuka, onse amene amakhala mʼmenemo amalira. Dziko lonse lidzadzaza ngati mtsinje wa Nailo, kenaka nʼkuphwera ngati mtsinje wa ku Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Ambuye Yehova wa makamu ndiye amene akhudza dziko, nilisungunuka; ndi onse okhalamo adzacita maliro; ndipo lidzakwera lonseli ngati madzi a m'nyanja; nilidzatsikanso ngati nyanja ya m'Aigupto;