Amos 9:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiwo amene amamanga malo ao okhalamo kumwamba, naika thambo ngati denga la dziko lapansi, amaitana madzi akunyanja naŵakhuthulira pa dziko lapansi. Iwowo dzina lao ndi Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndiye amene amanga zipinda zake zosanja m'mwamba, nakhazika tsindwi lake pa dziko lapansi; Iye amene aitana madzi a m'nyanja, nawatsanulira padziko; dzina lake ndiye Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye amene amamanga malo ake okhalamo kumwamba, ndi kuyika maziko ake pa dziko lapansi, Iye amene amayitana madzi a ku nyanja ndikuwakhuthulira pa dziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndiye amene amanga zipinda zace zosanja m'mwamba, nakhazika tsindwi lace pa dziko lapansi; Iye amene aitana madzi a m'nyanja, nawatsanulira padziko; dzina lace ndiye Yehova.