Amos 9:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Kwa Ine, Aisraelenu muli ngati Aetiopiya.” Akuterotu Chauta. “Kodi sindine uja ndidatulutsa Aisraele ku Ejipito? Kodi sindine uja ndidatulutsa Afilisti ku Kafitori ndi Asiriya ku Kiri?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kodi simukhala kwa Ine ngati ana a Kusi, inu ana a Israele? Ati Yehova. Sindinakweza Israele ndine, kumtulutsa m'dziko la Ejipito, ndi Afilisti ku Kafitori, ndi Aaramu ku Kiri?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kodi kwa Ine, inu Aisraeli, simuli chimodzimodzi ndi Akusi?” Akutero Yehova. “Kodi sindine amene ndinatulutsa Israeli ku Igupto, Afilisti ku Kafitori ndi Aaramu ku Kiri?
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kodi simukhala kwa Ine ngati ana a Kusi, inu ana a Israyeli? ati Yehova. Sindinakweza Israyeli ndine, kumturutsa m'dziko la Aigupto, ndi Afilisti ku Kafitori, ndi Aaramu ku Kiri?