Colossians 1:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwa Iyeyo Mulungu adafuna kuyanjanitsanso zinthu zonse ndi Iye mwini, zapansipano ndi za Kumwamba. Adachita zimenezi pakudzetsa mtendere kudzera mwa imfa ya Mwana wake pa mtanda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
mwa Iyenso kuyanjanitsa zinthu zonse kwa Iye mwini, atachita mtendere mwa mwazi wa mtanda wake; mwa Iyetu, kapena za padziko, kapena za m'Mwamba.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo kudzera mwa Iye Mulungu ayanjanitsenso zinthu zonse ndi Iye mwini, zinthu za pa dziko lapansi, kapena zinthu za kumwamba. Iye anachita mtendere kudzera mʼmagazi ake, wokhetsedwa pa mtanda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
mwa Iyenso kuyanjanitsa zinthu zonse kwa iye mwini, atacita mtendere mwa mwazi wa mtanda wace; mwa Iyetu, kapena za padziko, kapena za m'mwamba.