Colossians 1:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsopano ndakondwa kuti ndikukuvutikirani. Pakuti pakumva zoŵaŵazo, ndikutsiriza m'thupi mwanga zotsala za masautso a Khristu kuthandiza thupi lake, ndiye kuti Mpingo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsopano ndikondwera nazo zowawazo chifukwa cha inu, ndipo ndikwaniritsa zoperewera za chisautso cha Khristu m'thupi langa chifukwa cha thupi lake, ndilo Mpingowo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano ine ndikukondwa kuti ndinavutika chifukwa cha inu, ndipo ndikukwaniritsa mʼthupi langa zimene zikuperewera pa masautso a Khristu, chifukwa cha thupi lake, limene ndi Mpingo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsopano 1 ndikondwera nazo zowawazo cifukwa ca inu, ndipo 2 ndikwaniritsa zoperewera za cisautso ca Kristu m'thupi langa 3 cifukwa ca thupi lace, ndilo Eklesiayo;