Colossians 1:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Cholinga cha Mulungu ndi cha kudziŵitsa anthuwo kukoma kwake kwa chinsinsicho ndi ulemerero wake pakati pa anthu akunja. Chinsinsicho nchakuti Khristu ali mwa inu, ndipo Iye amakupatsani chiyembekezo cha kudzalandira ulemerero.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kwa iwo amene Mulungu anafuna kuwazindikiritsa ichi chimene chili chuma cha ulemerero wa chinsinsi pakati pa amitundu, ndiye Khristu mwa inu, chiyembekezo cha ulemerero;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa iwo amene Mulungu anawasankha kuti awadziwitse pakati pa a mitundu ina, ulemerero wa chuma cha chinsinsi ichi, amene ndi Khristu mwa inu, chiyembekezo cha ulemerero.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kwa iwo amene Mulungu anafuna kuwazindikiritsa ici 6 cimene ciri cuma ca ulemerero wa cinsinsi pakati pa amitundu, ndiye Kristu mwa inu, ciyembekezo ca ulemerero;