Colossians 2:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwa Iye mudachita ngati kuumbalidwa, osatitu kuumbala kwa anthuku ai, koma kuvula khalidwe lanu lokonda zoipa; kuumbala kumene amachita Khristu nkumeneku.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
amenenso munadulidwa mwa Iye ndi mdulidwe wosachitika ndi manja, m'mavulidwe a thupi, mu mdulidwe wa Khristu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mwa Iye inunso munachita mdulidwe mʼthupi lanu, osati mdulidwe ochitidwa ndi manja a anthu ayi, koma ochitidwa ndi Khristu pamene anavula khalidwe lanu lauchimo lija.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
amenenso munadulidwa mwa iye ndi mdulidwe wosacitika ndi manja, m'mabvulidwe a thupi, mu mdulidwe wa Kristu;