Colossians 2:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene mudabatizidwa, mudachita ngati kuikidwa m'manda pamodzi ndi Khristu. Ndipo ndi ubatizowo mudaukitsidwanso pamodzi naye, pakukhulupirira mphamvu za Mulungu amene adamuukitsa kwa akufa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
popeza munaikidwa m'manda pamodzi ndi Iye muubatizo, momwemonso munaukitsidwa pamodzi ndi Iye m'chikhulupiriro cha machitidwe a Mulungu, amene anamuukitsa Iye kwa akufa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mu ubatizo, munayikidwa mʼmanda pamodzi ndi Khristu ndi kuukitsidwa naye pamodzi, pokhulupirira mphamvu za Mulungu amene anamuukitsa kwa akufa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
popeza munaikidwa m'manda pamodzi ndi iye muubatizo, momwemonso munaukitsidwa pamodzindi iye m'cikhulupiriro ca macitidwe a Mulungu, amene anamuukitsa iye kwa akufa.