Colossians 2:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wina aliyense asakuzengeni mlandu pa nkhani yokhudza zakudya kapena zakumwa, kapena pa zokhudza masiku a chikondwerero, kapena a mwezi wokhala chatsopano, kapena pa zokhudza tsiku la Sabata.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake munthu aliyense asakuweruzeni inu m'chakudya, kapena chakumwa, kapena m'kunena tsiku la chikondwerero, kapena tsiku lokhala mwezi, kapena la Sabata;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake musalole wina aliyense kukuzengani mlandu chifukwa cha zimene mumadya kapena kumwa, kapena za masiku achikondwerero cha chipembedzo, za chikondwerero cha mwezi watsopano, kapena za tsiku la Sabata.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace munthu aliyense asakuweruzeni inu m'cakudya, kapena cakumwa, kapena m'kunena tsiku la phwando, kapena tsiku lokhala mwezi, kapena la Sabata;