Colossians 2:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wina aliyense asakuletseni kupata mphothoyo. Iwo aja amakonda kudziwonetsa ngati odzichepetsa, popembedza amatamanda angelo. Amaika mtima pa zimene akuti adaziwona m'masomphenya. Amadzitukumula popanda chifukwa, popeza kuti amangotsata nzeru za anthu,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthu aliyense asakunyengeni ndi kulanda mphotho yanu ndi kudzichepetsa mwini wake, ndi kugwadira kwa angelo, ndi kukhalira mu izi adaziona, wodzitukumula chabe ndi zolingalira za thupi lake, wosagwiritsa mutuwo,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musalole kuti wina aliyense amene amakonda kudzichepetsa mwachiphamaso ndi kumapembedza angelo akulepheretseni kukalandira mphotho. Munthu woteroyu amayankhulanso mwatsatanetsatane zinthu zimene akuti anaziona mʼmasomphenya. Anthuwa ndi odzitukumula ndi fundo zopanda pake zochokera mʼmaganizo mwawo amene si auzimu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthu ali yense asakunyengeni ndi kulanda mphotho yanu ndi kudzicepetsa mwini wace, ndikugwadira kwa angelo, ndi kukhalira mu izi adaziona, wodzitukumula cabe ndi zolingalira za thupi lace, wosagwiritsa mutuwo,