Colossians 2:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
osakangamira Khristu amene ali mutu wa Mpingo. Komatu mwa Khristu thupi lonse limalandira mphamvu, ndi kulumikizika pamodzi mwa mfundo zake ndi mitsempha yake. Motero thupi limakula monga momwe Mulungu afuna kuti likulire.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuchokera kwa Iye amene thupi lonse, lothandizidwa ndi kulumikizidwa pamodzi mwa mfundo ndi mitsempha, likula ndi makulidwe a Mulungu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo sakulumikizananso ndi mutu, kumene kumachokera thupi lonse, logwirizidwa ndi kumangiriridwa pamodzi ndi mʼmitsempha yake ndi mnofu, limene limakula monga mmene Mulungu afunira kuti likulire.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kucokera kwa iye amene thupi lonse, lothandizidwa ndi kulumikizidwa pamodzi mwa mfundo ndi mitsempa, likula ndi makulidwe a Mulungu.