Colossians 2:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mudafa pamodzi ndi Khristu, ndiye kuti simulamulidwanso ndi miyambo ya dziko lapansi. Tsono bwanji mukuchita ngati kuti moyo wanu ukudalirabe zapansipano? Bwanji mukuŵamvera malamulo onga aŵa akuti,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ngati munafa pamodzi ndi Khristu kusiyana nazo zoyamba za dziko lapansi, mugonjeranji kuzoikikazo, monga ngati moyo wanu mukhala nao m'dziko lapansi,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Popeza munafa pamodzi ndi Khristu kusiyana nayo miyambo ya dziko lapansi lino, nʼchifukwa chiyani mukukhalanso ngati a dziko lapansi lino? Bwanji mukumvera malamulo monga awa:
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ngati munafa pamodzi ndi Kristu kusiyana nazo zoyambaza dziko lapansi, mugonieranii ku zoikikazo, monga ngati moyo wanu mukhala nao m'dziko lapansi,