Colossians 2:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakuti ngakhale sindili nanu m'thupi, komabe mumtimamu ndili nanu pamodzi. Ndipo ndakondwa kuwona kuti mukulongosola bwino zonse, ndi kuti chikhulupiriro chanu mwa Khristu nchosagwedezeka konse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti ndingakhale ndili kwina m'thupi, komatu mumzimu ndili pamodzi ndi inu, wokondwera pakupenya makonzedwe anu, ndi chilimbiko cha chikhulupiriro chanu cha kwa Khristu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti ngakhale sindili pakati panu mʼthupi, ndili nanu pamodzi mu mzimu, ndipo ndikukondwa kuona kuti mukulongosola bwino zonse ndiponso kuti chikhulupiriro chanu mwa Khristu ndi chokhazikika ndithu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndingakhale ndiri kwina m'thupi, komatu mumzimu ndiri pamodzi ndi inu, wokondwera pakupenya makonzedwe anu, ndi cilimbiko ca cikhulupiriro canu ca kwa Kristu.