Colossians 2:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukhale ozika mizu mwa Iye. Mupitirire kumanga moyo wanu pa Iye. Mulimbike kukhulupirira monga momwe mudaphunzirira, ndipo muzikhala oyamika kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ozika mizu ndi omangirika mwa Iye, ndi okhazikika m'chikhulupiriro, monga munaphunzitsidwa, ndi kuchulukitsa chiyamiko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mukhale ozikika mizu mwa Iye, ndipo moyo wanu umangike pa Iye. Mulimbike mʼchikhulupiriro monga momwe munaphunzirira, ndipo kuyamika kwanu kusefukire.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ozika mizu ndi omangirika mwa iye, ndi okhazikika m'cikhulupiriro, monga munaphunzitsidwa, ndi kucurukitsa ciiyamiko.