Colossians 2:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chenjerani kuti wina aliyense angakusokonezeni ndi mau olongosola nzeru zapatali. Ameneŵa ndi mau onyenga chabe. Paja nzeru zimenezi zimangochokera ku miyambo ya anthu, ndi ku maganizo ao okhudza zapansipano, osati kwa Khristu ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Khristu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Musalole kuti wina aliyense akutengeni ukapolo ndi mʼnzeru zachinyengo zolongosola zinthu zozama, zomwe zimachokera ku miyambo ya anthu ndi ku maganizo awo okhudza za dziko lapansi osati kwa Khristu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati cuma, mwa kukonda nzeru kwace, ndi cinyengo copanda pace, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Kristu;