Colossians 3:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'moyo watsopanowu palibenso zoti uyu ndi Myuda kapena wosakhala Myuda, woumbala kapena wosaumbala, munthu wachilendo, munthu wosaphunzira, kapolo kapena mfulu, koma Khristu basi ndiye wopambana onse, ndipo amakhala mwa onse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamene palibe Mgriki ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, watchedwa wakunja, Mskuti, kapolo, mfulu, komatu Khristu ndiye zonse, ndi m'zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pano palibe kusiyana pakati pa Mgriki ndi Myuda, wochita mdulidwe ndi wosachita, wosaphunzira kapena wosachangamuka, kapolo kapena mfulu, koma Khristu yekha basi ndipo amakhala mwa onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamene palibe Mhelene ndi Ayuda, mdulidwe ndi kusadulidwa, wachedwa wakunja, Mskuti, kapolo, mfulu, komatu Kristu ndiye zonse, ndi m'zonse.