Colossians 3:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muzilezerana mtima, ndipo muzikhululukirana ngati wina ali nkanthu ndi mnzake. Monga Ambuye adakukhululukirani, inunso muzikhululukirana.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mulezerane mtima ndipo muzikhululukirana ngati wina ali ndi chifukwa ndi mnzake. Muzikhululukirana monga Ambuye anakhululukira inu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kulolerana wina ndi mnzace, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali naco cifukwa pa mnzace; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso;