Colossians 3:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iphani tsono zilakolako za mu mtima wanu woumirira zapansipano, monga dama, zonyansa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoipa, ndiponso kusirira zinthu mwaumbombo. Kusirira kotereku sikusiyana ndi kupembedza mafano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake fetsani ziwalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso chamanyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho, iphani zilakolako za dziko lapansi mwa inu, monga: dama, zodetsa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoyipa ndi umbombo, pakuti umbombo ndiko kupembedza mafano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace fetsani ziwalozo ziri padziko; dama, cidetso, cifunitso ca manyazi, cilakolako coipa, nelicisiriro, cimene ciri kupembedza mafano;