Colossians 4:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ifeyonso muzitipempherera kuti Mulungu atipatse mwai woti tilalike mau ake, makamaka kuti tilengeze chinsinsi chozama chokhudza Khristu. Chifukwa cha kulalika chinsinsichi ndine womangidwa m'ndende muno.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi kutipempherera ifenso pomwepo, kuti Mulungu atitsegulire ife pakhomo pa mau, kuti tilankhule chinsinsi cha Khristu; chimenenso ndikhalira m'ndende,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo muzitipemphereranso ife kuti Mulungu atitsekulire khomo la uthenga wathu, kuti tilalikire chinsinsi cha Khristu, chimene ndine womangidwa nacho mʼndende.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi kutipempherera ifenso pomwepo, kuti Mulungu atitsegulire ife pakhomo pa mau, kuti tilankhule cinsinsi ca Kristu; cimenenso ndikhalira m'ndende,