Daniel 1:10 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nati mkulu wa adindo kwa Daniele, Ine ndiopa mbuyanga mfumu, amene anakuikirani chakudya chanu ndi chakumwa chanu; pakuti aonerenji nkhope zanu zachisoni zoposa za anyamata olingana ndi inu? Momwemo mudzapalamulitsa mutu wanga kwa mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
koma ndunayo inamuwuza Danieli kuti, “Ine ndikuchita mantha ndi mbuye wanga mfumu, amene wapereka chakudya ndi chakumwa chanu. Kodi akuoneni inu owonda kuposa anzanu a misinkhu yanu pa chifukwa chanji? Mfumu ikhoza kundidula mutu chifukwa cha iwe.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nati mkuru wa adindo kwa Danieli. Ine ndiopa mbuyanga mfumu, amene anakuikirani cakudya canu ndi cakumwa canu; pakuti aonerenji nkhope zanu zacisoni zoposa za anyamata olingana ndi inu? momwemo mudzaparamulitsa mutu wanga kwa mfumu.