Daniel 1:17 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma anyamata amene anai, Mulungu anawapatsa chidziwitso ndi luntha la m'mabuku ali onse, ndi nzeru; koma Daniele anali nalo luntha la m'masomphenya ndi maloto onse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kwa anyamata anayiwa Mulungu anapereka chidziwitso ndi kuzindikira bwino mitundu yonse ya zolembedwa ndi za maphunziro. Ndipo Danieli ankatanthauzira masomphenya ndi maloto a mitundu yonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma anyamata amene anai, Mulungu anawapatsa cidziwitso ndi luntha la m'mabuku ali onse, ndi nzeru; koma Danieli anali nalo luntha la m'masomphenya ndi maloto onse.