Daniel 1:2 — Compare Translations
3 translations compared side by side
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anapereka Yehoyakimu mfumu ya Yuda, m'dzanja lake, pamodzi ndi zipangizo zina za m'nyumba ya Mulungu, namuka nazo iye kudziko la Sinara, kunyumba ya mulungu wake, nalonga zipangizozo m'nyumba ya chuma cha mulungu wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Ambuye anapereka Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda mʼdzanja lake, pamodzi ndi zina mwa zida zotumikira mʼNyumba ya Mulungu. Iye anazitenga napita nazo ku nyumba ya mulungu wake ku Babuloni ndi kuziyika mʼnyumba yosungiramo chuma cha mulungu wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anapereka Yehoyakimu mfumu ya Yuda, m'dzanja lace, pamodzi ndi zipangizo zina za m'nyumba ya Mulungu, namuka nazo iye ku dziko la Sinara, ku nyumba ya mulungu wace, nalonga zipangizozo m'nyumba ya cuma ca mulungu wace.